24/04/2026
0888892375/WhatsApp:
Kodi Nchifukwa Chani Tikuvutika ndi Nkhani ya Mabatile?
AMalaŵi anzanga galimoto ili yonse ili ndi batile lake loyenereka. Batile loyenereka limapereka mphamvu zoyenerera ngakhale kutadzidzira chotani kuti galimoto ilire. Batile lirilonse lomwe a Malawi Bureau of Standards (MBS) alirola kuti lilowe ku Malawi kuno liyenera kukhala (marked) ndi mphamvu yake yopukutsira ingini kukadzidzira kwambiri (Cold Cranking Amps -CCA).
Vuto limene tili nalo ndi loti sitidziwa batile loyenerera galimoto yathu ndiye timangogula lina lirilonse. Amene mumagula magalimoto ochoka kunja monga ku Japan onetsetsani kuti batile limene liri mugalimoto ndi lotani. Mupeze mphamvu zake. Apa mupeze chimene timati mphamvu pa ola (Ampere hour -Ah) cha batile limene labwera ndi galimotoyo. Chonde musaone kukula kwa batile (physical size) chifukwa monga kukula kwa N50 pali mphamvu pa ola zosiyanasiyana monga 50Ah, 55Ah, 60Ah, 65Ah, 70Ah...
Chimodzimodzinso kukula kwa N70 pali 70Ah, 75Ah, 80Ah, 90Ah, 95Ah...Ife athu panopa ndi ma 95Ah.
Mwachidule mabatile sitigulitsa ngati tomato.
Mukafuna zambiri kuti muthandizidwe moyenerera tipezeni pa 0888892375/WhatsApp. Miyezi 18 kapena 9 ya warranty ngati tayeza galimoto yanu ndipo yakhoza. Mudzibweranso miyezi itatu iliyonse kudzatcheketsa.